Maliro Ndi Miyambo Ya Chewa
Maliro Ndi Miyambo Ya Chewa
la Chiwiri
Archibald J. Makumbi
Chiyamiko
Ndiyamika Boma la Malawi pondilola kulemba bukuli, makamaka Bungwe lija la
‘African Book Selection Committee, pondichitira chifundo.
Zikomo kwa Rev. Amoni Dembo Mvula amene adalola kundiuza zina zakale,
ndikutinso adandilimbikitsa pamene ndidayamba kufooka.
Mayamiko anga apitenso kwa akulu a DRCM Nkhoma, amene adandilola kukaona
ku chipinda chosungira zakale.
AJ Makumbi
1
Zam’kati
Mawu oyamba Tsamba
1 Maliro a mwana wofera m’chikuta
2 Mwana wamasiku kapena miyezi
3 Mwana wamtengwa
4 Kubadwa kwa mwana*
5 Mwana woyamba kumera mano kumwamba
6 Maleredwe a ana a Achewa
7 Mwana wamasiye
8 Mnyamata
9 Mayi wolowa kudambwe*
10 Mayina a gule wamkulu*
11 Mtsikana akapeza bwenzi*
12 Chinamwali
13 Namwali akatha msinkhu
14 Mkazi wachitengwa
15 Mkazi akakhala ndipakati
16 Maliro a mkazi wosiya mwana pobereka
17 Munthu wakhate
18 Munthu wodwala nthomba
19 Uzimba
20 Kapolo
21 Za ufiti, mankhwala ndi matsenga
22 Masasa
23 Munthu wofa ndi mankhwala
24 Maliro a munthu womwa mwavi
25 Maliro a munthu wachuma
26 Munthu wophedwa mwangozi
27 Maliro a munthu wofa mwadzidzidzi
28 Maliro a munthu wakhunyu
29 Munthu wopsa ndi moto
30 Munthu wodzipha yekha
2
31 Maliro a chitsiru
32 Mdulo (tsempho)
33 Maliro a mkamwini
34 Maliro a namkungwi
35 Maliro a nduna ya mfumu
36 Maliro a mfumu ya mzinda
37 Ufumu wa Achewa*
38 Mawu otsiriza
38
3
Mawu oyamba
Cholembera bukuli n’choti tilondole za miyambo ya Achewa kuti mbiriyi
isungidwe kuti ana am’tsogolo adzaidziwe.
Anthu a mu Africa ambiri ndiwo ‘Abantu’ amene amakhala kumwera, kuvuma ndi
kuzambwe kwa Africa.
Ndipo popeza kuti Achewa ndi limodzi mwamagulu a mtundu wa Abantu, ndifuna
kulondola maliro ndi miyambo ya Achewa, ndi mmene iwo amasamalira
miyamboyo.
4
Cholinga cha bukuli
Ganizo loti ndilembe bukuli litandifikira ndidaganiza kuti ndidayenera kuyamba
ndalowa kudambwe kuti ndidziwe zambiri za gule wamkulu. Ndipo ndisadalowe
ndidayambabe kulemba bukuli ngakhale mfundo zake zidali zogendagenda.
Nthawiyi idali chaka cha 1946 ndipo bukuli lidatuluka 1948, ndipo wolisindikiza
adali a Longman – Green Company Limited ku United Kingdom. Bukuli litatuluka
mafumu a mzinda adakhumudwa nalo ndipo zotsatira zake zidali zogula mabuku
onse ndi kuwatentha, motero padali adani awiri, mpingo ndi amizinda. Pofuna kuti
ndidziwe kwambiri za gule wamkulu ndidapempha chilolezo kumpingo wanga kuti
ndilowe kudambwe koma adandikaniza koma popeza ndidali ndi cholinga,
m’chaka cha 1970 ndidakalowabe kudambwe. Mosataya nthawi ndidaphunzira
zambiri panthawi yochepa ndipo ndidatulukako m’chaka cha 1980.
5
Pamene mkazi ali wodwala pakati pamakhala miyambo ndi chisamaliro chambiri.
Panthawiyi mkaziyo saloledwa kuyang’ana mtembo wa munthu wakufa kuti
angadzabereke mwana wamzukwa. Koma ndi zomvetsa chisoni kuti amagwira
ntchito zolemetsa, mwinanso kumenyedwa ndi mwamuna wake ngati alakwa.
Mwamunayo saloledwa kuyenda ndi akazi ena, kapenanso kuyendera mitala yake,
kuti angadule mkaziyo. Ndiponso saloledwa kukumba manda mpaka mkaziyo
atadzakhala bwino.
Ataika malirowo amayi onse amatenga mitsuko yawo napita kumadzi, nakasamba
kukachotsa ziwanda. Akafika kumudzi, amatenga makasu nawaula ndi moto;
amatero kuti ziwanda zingatsalire kumakasuwo.
Ndipo kukakhala kuti mkaziyo wapita pachabe kawiri kapena katatu, pamakhala
mlandu wakuti mwamuna sali kuyenda bwino, bwanji mkazi angopita pachabe
nthawi zonse. Mwa ici, ankhoswe akuchimuna ndi akuchikazi amakumana
nakamba mlanduwo, ndipo amalipira mbuzi, ndiko kuti mzimu umene ulikupha
anawo ukhululuke. Patsiku lometa amatenga nkhuku naponya m’nyumbamo.
6
Dzina la nkhukuyo amati, ‘nkhuku yakumitu’ ndipo amadya ndi ana okha a
m’nyumbamo.
Pamaliro awa pali imfa zosiyanasiyana. Zifukwa zake za imfayi tanena kale kuti
Abantu sadadziwe makhalidwe olongosoka, ngati ukhondo ndi chakudya
choyenera, choncho amachita zambiri mosalongosoka.
Pali mbiri yakuti ku England kukabadwa ana zana limodzi (100), ndiponso kuno
ku Africa kwabadwanso ana 100, ana 40 a ku Africa amamwalira isanathe miyezi
isanu ndi umodzi, koma a ku England amamwalira mwina anayi okha patapita zaka
zambiri.
7
Atatha zonsezi amapita kumudzi nakatenga mtembo, ndipo amaliranso kwambiri
podziwa kuti tsopano mwanayo ali kukaikidwa kumanda ndipo sitidzamuonanso.
Mwana wamtengwa
Kalelo mwamuna sankaloledwa kutenga mkazi kupita naye kwawo ngati ntchito
zake sizidali zokwanira kusunga munthu. Ndiponso ngati m’banjamo mulibe
mwana, popeza amayi a mkazi amati, ‘Sitidziwa, mwina mwamunayo
ngosabereka.’ Choncho ngati iye sankaonetsa izi sankaloledwa konse kutenga
‘chitengwa’. Zitengwa zilipo zamitundu iwiri: chitengwa chodziwana bwino ndi
ankhoswe akuchimuna ndi akuchikazi, ndi chongomvana mwamuna ndi mkazi
wake.
Ankhoswe aja amapitadi kwa anzawo aja nati, ‘Pepani anzathu, ife timafuna kuti
mkaziyu akatiphikire kwathu.’ Ndipo ankhoswe akuchikazi amauza nkhaniyi
makolo a mkaziyo. Atavomerezana, amati, ‘Chabwino, wathuyu tengani, koma
pakaoneka matenda ndi zovuta zina muzidzatiuza mofulumira.’
8
akudwala. Nthawi zina mwana amadwala mwadzidzidzi ndipo pasanapite masiku
mwanayo amamwalira. Mwankhawa, amatumiza mthenga wokanena kwawo kwa
mkazi kuti mwana wa mwana wanu uja amwalira.
Choyambirira kuyamba ndi banja. Kuti banja liyambike ndiye kuti mwamuna ndi
mkazi akambirana zachibwenzi chodzadzetsa banja. Atagwirizana mnyamata
amadziwitsa atsibweni ake (malume) za nkhaniyo. Mosazengereza atsibweni aja
mwina amatuma wina kuti akafunsire mbeta. Atafika kumudzi kuja amamulonjera
motere: ‘Monitu.’ Iye amayankha kuti, “Ee moni.” ‘Nanga n’kwabwino?’ Iye
9
amati, “Ee n’kwabwino.” Kenaka amamfunsa kuti, ‘Nanga mwatiyendera?’
“Zoonadi tadzakuyenderani. Koma chodzera kunotu n’chakuti, kwathuku tili ndi
tambala ndiye timati tidzasinthane ndi msoti wanu,” iyeyu amayankha motero.
Mwana
Mwana akabadwa, chodziwitsa kuti mwanayo ndi wamoyo amalira kuti, ‘Ng’a!
Ng’a! Ng’a!’ Mosazengereza amanjata mchombo wa kamwanako kuti mphepo
ingamulowe m’mimba. Amayi amatenga chipande n’kuthiramo ufa ndi madzi
n’kumatakasa ndi chala chamkombaphala mosaliika pamoto konse. Akasakaniza,
amagadamitsa mwanayo ndi kumumwetsera pachikhato. Kenaka amamusambitsa.
Zikatero amaimba nthungululu kuti mfumu idziwe, komanso mudzi onse. Kenaka
namkungwi amakadziwitsa mfumu motere: “Odi, amfumu!” Mfumu imayankha
kuti, “Odini.” Ikatero imatsegula chitseko ndikunena kuti, “Lowani.” Namkungwi
10
atalowa mfumu imati, “Tikuoneni.” Namkungwi amati, “Zikomo amfumu.”
Mfumu imati, “Kodi n’kwabwino?” “N’kwabwino. Kutereku n’kudzakudziwitsani
kuti, mwana uja anali wodwalayu tsono wakhala tsonga.” Mfumu imati, “Kodi,
zikatero zakhala bwino. Kuteroko kuli munthu wamtundu wanji?” “Ndithu,
kwabadwa munthu wamwamuna,” nankungwiyo amatero. Mfumu imati, “Zikomo
kwambiri. Umo ndimo zinthu zimayenera kukhalira. Nanga makeyo ali bwanji?”
“Ali bwinobwino ndithu wopandanso kamtsaliro.’ Mfumu imati, “Kodi! Zakhala
bwino.”
Dzina Tanthauzo
Tobalire kwangovutika kubereka
Tankhulenji chonena tilibe
Tafatatha tangotitsirizani
Chipezayani ine ndiye ndatsogolako
Balalata chidzakupeza
Phereni ndekha sindingathe
Nkafanikhale zivute zitani sindidzaopa
Kapazam’mbali wamaganizo opotoka
Kamwendom’njira wosakhazikika pamalo amodzi
Titani tigwira mtengo wanji
Chimkondenji mutopa kukamba za ine
Chapansi kubisalira
Mumderanji ndimalakwanji
Mwathaanansi mwatsala nokha
Zayakunkhongo wosaweruzika
Kulinji wosalabadira zam’tsogolo
Kumvenji kumbuyo kulibe maso
Mawuawawa mawu owawa aposa saiwalika
Mtisunge tikhale nawo musatitaye
Mtengaponji palibe chomwe mupindulepo
Mferamo mwangoferamo opanda mwana
Zagwazatha zachitika kale
Kangachepe ndikwanitsa musandiderere
Katsonga kupezapo bwino
Mwalipeza mudzatikumbukira
11
Mzati mlimbiko pogomezera
Dalitso mphatso yaulere
Munguuza wosowa nansi
Kathewera chovala m’chiuno mokha
Msasata ndalira ena
Mphindapansi zolowere n’kudyere mwana
Zimpita wosaweruzika
Mwaonanji mudandileka kale
Kamzunguze mpitireni pansi musamuuza
Bololo sakondamadzi simungandithe
Mwadzaangati mwachepa
Mkalinacho chidani chamgonamgona
Chikalipo kusungira zinthu mumtima
Sulitha zikukanika
Msekamwamvu womana kapena wosamverana chisoni
Masautso kusowetsa mtendere
Msekadala chikondi chachinyengo
Mlimbanaye suyotu mumuona nokha
Sindisamala chichitikechichitike
Sosola pitikitsani kapena chotsani
Mtalimanja munthu wosasowa kanthu
Chosadziwa zosakonzekera kuti zichitika
Tchete kavuwevuwe
Kanthun’kako kusadalira za ena
Mthyoka wolumala ziwalo
Mzembera wosanena zoona
Mphungusatayanthenga wakaligwiritsa
Kayendekeza woyembekezera ufumu
12
Maso m’masomu mumakhala kapena mumatuluka manthongo,
kenaka maso amafiira, ndi kuwawa kwambiri.
Ukweche m’phechepeche mwa mwana mumatuluka matuza oyera
ndiponso onyenyesa zedi.
Utumbidwa (tsempho) mwana wooneka wosasangalala, komanso wopanda
chilakolako chakuti adye. Thupi lake looneka ngati lidawawuka
ndi moto. Mimba imauma komanso miyendo imatupa.
Mphala
Pamudzi ulionse pamakhala kanyumba kena kodziwika ndi dzina lakuti mphala.
Nyumba imeneyi ndi ya anyamata ang’onoang’ono amene sadakwatire. Pamene
mwana wakula ndithu amamutumiza kwa agogo ake. Atasunzunukapo, ngati ndi
mnyamata amakagona kumphala kwa anzake. Anyamata amagonera ndi kudyera
limodzi ndipo usiku amaphunzitsana nthano, miyambi ndi zina. Nyumbayo
imakhala ngati sukulu yophunziriramo maluso osiyanasiyana, monga kuweta
ng’ombe, mbuzi, nkhosa; kumweta tsekera ndi kuphunzitsana kumanga mfundo
yachimuna. Pakakhala makangano, amaweruzana bwinobwino potsutsa wolakwa.
Pamakhala ena okulirapo omwe amakhala ngati atsogoleri. Komanso kumeneko
kumakhala kuphunzitsana maudindo monga kutolera nkhuni, kuweta ziweto ndi
masewero ena olimbitsa matupi. Pali chikhulupiriro choti ana ogona m’mphala
amakula bwino ndipo amakhala olimba m’thupi, aulemu, omvera, antchito ndi
ochangamuka.
Alipo ana ena amene amathawa kumphala nabwerera kwa makolo awo. Oterewa
amawaseka. Zikatero mwana wotero amamusala nakhala ndipo amakhala
chiyendayekha. Pakudya nsima, mwana sayenera kuyamba kusamba. Kumphala
kumakhala chidyerano, womwe ndi mchitidwe wosonkhanitsa nsima zonse
m’mphalamo n’kumadyera limodzi. Ana amaonetsa osakhuta msanga malinga
n’kubadwa kwawo.
13
Kuka
Achewa ataona kuti m’banja lina mwabadwa mwana, koma pomera mano ayamba
kumwamba, makolo ake amwanayo amapita msanga kwa mfumu nam’dziwitsa
zonse za mwanayo. Pakati pa Achewa amaganiza kuti mwana wotere adzakhala
mfiti, wodya anthu ndiponso wosatsutsidwa. Podziwa ichi, samalola mwana
kukhala pakati pawo.
14
Maliro otere samawalira kapena kugonera pamtanda, koma amangochita ngati
ataya galu wachiwewe.
Komanso sizikudziwika ngati makolo a mwanayo amakondwera ndi mchitidwewu.
Achewa adali ndi miyambo yolerera ana awo. Ndipo m’mutuwu munenedwa
mwachidule miyambo ina ya Achewa yokhudza maleredwe ya ana monga iyi:
15
• Mnyamata akagwaza mnzake ndi chisongole chosokera mphasa ndiye kuti
wolasidwayo amayenera kutenga nkhuku yoyera napatsa amene
anamugwazayo.
• Mwana ayenera kudya dothi kuti atsendere liombo (msoma).
• Mwana akamalira pamene mayi ali patchito yolima kapena yophika, wina
amulande mayiyo khasulo kukhala lake, kaya ngati akuphika, amulande
nsimayo. Amatero popeza kuti kuteroko ndi kuzunza mwana.
• Mwana avekedwe mkanda pakhosi, pamiyendo, pamanja ndi m’chiuno.
Womutcha dzina am’patsenso mkanda.
Mwana wamasiye
16
M’dziko lonse lapansi pamaoneka ana amasiye. Pakati pa Achewa ana amasiye
adalipo, koma kasamalidwe kapena machitidwe ake amasiyana ndi mmene
imachitira mitundu ina ya anthu.
Pamene mayi wamwalira amasiya ana pabanja. Anawa amasauka kwambiri popeza
mabanja ena amawakana kuwalera nati, ‘Nditha kulera ana amasiye, koma pamene
mzimu wa mayi wawo ubwera kufuna ana akewo utha kudzatenga mwana wina,
mwina m’malo motenga mwana wamasiyeyo ungadzatenge mmodzi mwa ana
anga.’ China ndichakuti amaopa kulongosola ana amasiyewo.
Mnyamata
Mnyamata akakula, makolo ndi amalume ake amapangana kuti mnyamata ayenera
kupita ku nyawu. Uyu ndi gule wa Achewa amene amachita panthawi yamaliro
yokha. Monga mudziwa nyawu zilikuchuluka kwambiri m’maboma awa:
Lilongwe, Dowa, Kasungu, Nkhotakota, Ntchisi, Mchinji, ndi Dedza, popeza
kumeneku ndiko kuchimake kwa Achewa.
Nyawu imapangidwa ndi zinthu monga izi: makoko, udzu, luzi, ndi chibzero.
Akalowa mnyamatayo amadabwa kwambiri, popeza asanabwere kudambwe
(kumalo kumene amapangira nyawu) amauzidwa kuti nyawu ndi nyama yamafuta
imene amaitulutsa padziwe ndi mbeza ndipo nyambo yake ndi dzira. Koma pa
nthawiyi iye amaona kuti zonse zimene adamva zidali zonama.
17
Zikatero ku dambweko akuluakulu amamenya anyamatawo zolimba, ndipo ena
amavulala kwambiri. Amatenga mnyamata, namutulutsa m’nyuwu, nayamba
kum’menya kwambiri. Makolo a mnyamatayo amaneneratu zimene mnyamatayo
amachita, zabwino kapena zoipa, zamwano kapenanso zaulemu.
Akatha izi amayamba kumuuza miyambo ndi malango a nyawu nati, ‘Mum’phika
wa amayi ako osakapisamo manja; kubedi kwa makolo ako osamakapitako;
osakakhala pamodzi ndi amayi ako; ndiponso osakasewera ndi ana aang’ono.’
18
Yankho: phulusa (chipala)
• Magazi anyawu n’chiyani?
Yankho: thukuta lamunthu
• Mtima wa nyawu n’chiyani?
Yankho: munthu
• Kautsa gule n’chiyani?
Yankho: chabzero
• Nthiti yagule n’chiyani?
Yankho: chabzero
• ‘Ithani gule’
Yankho: namkungwi, chilale, thonje, makhwatha
• Pansipo!
Tanthauzo: wovinitsa nyawuyo wanyamulitsa ndipo atsitse pansi mmene
mwalowa nyawuyo
• Chalunda chosaguba
Tanthauzo: chaola munthu sameta chosamvera
• Tidzaonana podya mphonda
Tanthauzo: tsiku limene kudzakhale gule tidzakukhaulitsa kapena
udzamenyedwa
19
Mnyamata wokalowerera kudambwe
Ng’oma zitatha namwali amakhala kusimba ndi phungu wake, ndipo chakudya
amamutengera ndi phungu uja tsiku ndi tsiku mpaka tsiku loombetsa m’manja
litakwana.
20
amapolokeza. Ntchito ya mayiyo (udindo) n’kupezera zosoweka kudambweko,
monga phala, ufa, nkhuku ndi mowa zochokera kumudzi. Ngati pali zoyenera
kuphika kudambweko umakhalanso udindo wake.
Patsiku loshambula mowa ndi patsiku lotsiriza pamene zilombo zonse zimavina
masana, mayiyo amavina nawo m’bwalomo ndipo amasupidwa ngati chilombo
chomwe.
Tsono mpingo ndi gulu la anthu amene ali ndi chikhulupiriro ndi chiphunzitso
chimodzi ndiponso amachita mwambo wosonyeza kulowa kapena kulandilidwa
mugulumo, monga ubatizo kwa Mkhirisitu. Angakhale anyawu angafanane ndi
mpingo pazimene tanenapa, sasonyeza chipembedzo. Angofanana ndi gulu limodzi
m’mpingo wa Chikhirisitu.
Pajathu mpingo kapena gulu limakhala ngati banja kapena ana anyumba imodzi pa
khalidwe ndi zochitika zawo. Tsono wochita zosiyana mwina zosutsana ndi anzake
kapena amene sali ndi mbali mu upowo ndi wakunja. Ichi chikutanthauza kuti
ampingo umodzi atha kunena wa mpingo wina kuti ndi wakunja, kapena a gule
wamkulu atha kutchula Mkhiristu kuti ndi wakunja, Akhirisitunso chimodzimodzi.
Mayina a gulewamkulu
Njovu
Gule ameneyu ndi wamkulu kupambana magule ena onse. Ndiye satuluka wamba
kaya kuti chisawawa koma pokhapokha pa maliro a mfumu, nduna ndi a
namkungwi, komanso amatuluka pamkangali. Dambwe la Njovu ndi la mafumu
okhaokha. Mnyamata saloledwa kukhalira nawo popanda kupereka nkhuku.
21
M’nsupo wake ndi ng’ombe, mbuzi ndi kufundika mphasa pa msana. Nyimbo yake
amati:
Pang’onopang’ono abambo ogo ee!
Pang’onopang’ono abambo ogo dede!
Wochita mang’ombe amati: Hee, hee!
Njovu
Mdondo
22
Mdondo
Kasiyamaliro
Iyi ndi nyawu yokongola kwambiri komanso amayipanga bwino zedi mwaluso.
Patsiku lotulutsa Njovu, Kasiyamaliroyo amatsogolera Njovuyo. Kubwalo
imayamba kuvina ndi Njovuyo. Nyimbo yake imvekere:
Chimcheka dede! Kasiya eede.
Othirira mang’ombe n’kumati:
Kasiyamaliro ee hehe!
Kasiyamaliro
23
Kasiyamaliro
Kalulu mkuluwabwalo
Chadzunda
Nyimbo yake amati, “Kumalambo dedede he- he- he-he! Kumalambo dede!
Tinkanena dede! Tinkanena dede hehehe!”
24
Chadzunda
Kadyankhadze
Chimaoneka m’maliro masana, dzuwa likuswa mtengo. Nyimbo yake ina imati:
“Odede, dedza hoo! Odede, dedza ayo! Inde inde tate adagwa m’chipala!”
Kadyankhadze amavala kabudula ndi Malaya agwanda.
Simoni
25
Maonekedwe aguleyu amafanana ndi a Kadyankhadze, kusiyana kwake n’kuti
amaneyu amavala buluku. Komanso kuvina kwake satumphatumpha ngati
Kadyankhadze uja koma amavina cham’mbali. Kumaso kwake kumakhala kofiira
mochititsa mantha ndipo amayenda ndi nkhwangwa ya katemo, kosiyanapo ndi ija
timadulira mitengo.
Simoni
Chimtabwa (Mapulanga)
Nyawuyi imakhala ndi milomo yaitali kwambiri ndi mano aataliatali mbali zonse
ziwiri. Mkamwa mwake mumaoneka ngati moto poyenda ndipo povina
chimatenga misikiri iwiri, n’kumaiombetsa n’kumamveka kuti ngwi, ngwi.
Chimavina mbali zonse ziwiri chakutsogolo ndi kumbuyo.
26
Namyikwi
Palambwe
Chilombo chachikulu mutu, wongoti thasaa. Ndiye pali nyimbo imati, “Bwerekeni
nkhwangwa n’katemere pamutu Palambwe ee! Chitandale ee! Chitandale!” Ena
amati, “Nkhwangwayo, eyaye! Kaliyaliya siyako njobwereka! Pamutu palambwe
aleke wana asewere!”
Kasinja
Pali akasinja amitundu iwiri: Kasinja wausiku ndi wamasana. Kasinja amavala
thupi lonse ndi zigodera zina zam’khosi ndi za m’chiuno, ndipo mavinidwe ake
ndiolingana. Nyimbo zakenso n’zofanana. Mwa nyimbo zake ina amati, “Olekeni
ochoke! Koto koto! Asiyireni mwana yekhayo, olekeni ochoke!”
Kapoli
Maonkedwe ake sasiyana kwambiri ndi a Kasinja. Kapoli ali ndi mawu aang’ono
koma ogalamula kwambiri ndipo mavinidwe ake ndi yokondweretsa. Nthawi
imene chikuvina amachiyimbira salamba, m’mbalimu anyamata
akuchitchetcherera mochizungulira, atavala maseche munthanthula. Amayi
nthungululu zili pakamwa, wosupa akusupa chilombocho komanso uja wa tseche
wotchetcherera.
27
Kapoli
Vinsabwe
Vinsabwe
Kudambwe
Uku ndi kumalo kumene kumachokera nyawu zonse. Kumeneku ndiko kuchipala
kwa gule wamkulu. Amasankhula ku mtsinje, kukhwawa kapena kumanda. Pa
tsiku loyamba gule mwini maliro amafunsidwa kupereka chakudya cha tsikulo;
28
ndiwo ndi ufa. Dzina lake amati ‘chipondadambwe’, ndipo chakudyachi
chimaphikidwa komweko. Chakudyacho chimakhala cha eni mudzi.
Chimbano
Chimbano
Malamulo a kudambwe
29
Izi zonse ndizoletsedwa, ndipo sizisiyana konse ndi malamulo khumi aja a
Mulungu.
Masiku ano zinthu zasintha. Wachigololo ndi wakuba sakuphedwa konse. Koma
kale m’malo mwa malamulo amenewa m’mudzi munali bata ndi mtendere, ndi
umodzi. Kusinthaku kwadza chifukwa cha kumvera kwa anyamata.
30
naye kumtengo wa anamwali, ukonso kumasonkhana anamkungwi onse amidzi
yozungulira. Namkungwi wapamudzipo, ndiye amatumiza mauthenga.
Anamkungwi aja ntchito yawo ndi yophunzitsa namwali mavinidwe, maphikidwe,
magonedwe, osaiwalanso miyambo.
Masiku a mkangali amakhala atatu. Tsiku loyamba amati chiuluulu ndipo mtsikana
amavekedwa kulekeza mchiuno, mawere pamtunda ndipo m’mutu amamuveka luzi
kapena mlaza.
Anamwali
Chitengwa
31
zopita kwawo. Asadafunse ankhoswe za chitengwa poyambirira amagundana
zifuwa ndi mkaziyo. Akagwirizana amakauza ankhoswe akuchimuna
kudzapempha chitengwa. Asadayankhe, amakhala naye pansi wawo uja.
Atavomereza motsimikiza mtima akuchimuna amaitanidwa nawauza kuti, ‘Nkhani
yanu idamveka chotsatira tipatseni nkhuku yachitengwa.’ Koma ngati mnyamata
amachita zabwino, mfumu pamudzipo imakana kuti mnyamatayo asachoke.
Chikumu
32
nkhukuzo. Mawu achiwiri amati, ‘Tipatseni chizungulirakhonde. Mutipatse mbuzi
zitatu, koma cha mfumu mutipatsa nkhuku ziwiri ndiponso chiongo
mutikumbukire bwino lino. Tsonotu ndi msoti wa ng’ombe.’
Chinamwali (Mkangali)
Atasinja tsiku linalo amayamba mowa, kapena kuti kufulula mowa. M’mawa
mwake amaphika mowa uja. Kutada kumamveka kulira kwa nkhandwe
ponseponse kuti, ‘Bwe! Bwe!’ Ndi kubangula kwa mikango ponseponse. Ichi ndi
chisonyezo choti mawa chinamwali chiyamba. Mithenga imapita kumidzi
yozungulira, ndipo madambwe onse amatumiza nkhandwe ndi mikango
kuchinamwaliko.
33
Ena amayimba nthungululu. Izi zimachitika mpaka m’matandakucha. Kutacha,
m’mawa midzi yonse yozungulira mudzi womwe kuli mkangali amakhalira gule
kumadambwe osiyanasiyana. Tsikuli amayi amavina chiuluulu ndipo yemwe
amayamba ndi phungu kapena namkungwi, mafumu ali pa mphasa, ali kuonera ndi
kusupa. Anamwali amavina bwino lake, atayamba amaonera chitsanzo cha
aphungu ndi anamkungwi. Kutada usiku, gule amavina ndi zilombo, monga
Kapoli, Kasinja, Makanja ndi Pedegu.
Gule atatha, zilombo zina pamodzi ndi namwali uja amatsogolera kupita ku madzi.
Atafika uko namwali amauzidwa kusamba. Kusamba kwake kumakhala posamba
m’chiuno, miyendo, nganga kuphatikiza mabere, manja ndi mutu, pomwe kwina
ndi kusamba thupi lonse. Amayi amalangiza namwali masambidwe aziwalo zonse
za thupi lonse lachikazi, uku ndi kuphunzitsa ukhondo. Patsiku lachiwiri
pamakhalanso kuvina mjedza, ndi potsirizira amayi amafikanso ndi namwali kuti
adzavine.
Mwambo wa fisi
Anthu amasankha mnyamata mwachinsinsi kuti akhale fisi, ngati namwaliyo ndi
wosakwatiwa, kuti akhale ngati mwamuna wake. Mnyamatayo amatchedwa ‘fisi’
popeza amafika nthawi yausiku yokha. Fisiyo amachoka kumbandakucha, kotero
anthu ena sadziwa za iyeyo. Fisi ntchito yake ndi kuyesa mtsikana za chinamwali
34
chake. Atafika fisi uja amalandiridwa ndipo amagwira ntchito imene wadzera
mpaka masiku angapo, ndipo atatha amapatsidwa malipiro omwe adalonjezana
ndipo zonse zimathera pomwepo. Fisi samaloledwa kubweranso.
Nthawi zina ngati malipiro asowa amati, ‘Fisi akagwira mbuzi sataya,’
amangotengeratu namwaliyo. Komanso angakhale malipiro ataperekedwa,
mnyamatayo amamvana ndi mtsikana kuti lingokhala banja. Nkhoswe zambali
zonse ziwiri zimakumana n’kupatsana zofunikira monga chiwongo kapena
chaliombo. Ena amati ‘kumuonga’ (kuthokoza). Izi zimakondweretsa makolo kuti
kupatukana mbanjamo kwatha ndipo ali omasuka kugonera limodzi pakati pa
mwamuna ndi mkazi wake monga kale. Dzina lina lakupatukanaku amati,
‘dongosolo’.
Mkangali
Chinamwali cha mkangali ndi chinamwali choyamba ndiponso chovomerezeka.
Mkangali ndi chinamwali cha atsikana ndipo chiyambi chake chimakhala chakuti
mtsikana akathyola bano, kapena kutha msinkhu, mfumu imauzidwa kudzera kwa
namkungwi. Ntchembere zimakumana kunyumba kwa mtsikanayo kumuuza ndi
kumulangiza miyambo mpaka tsiku lomaliza msambo. Malangizo ake amatere;
‘Tsopano wakula ndiye osamasewera ndi anyamata kuti ungatenge mimba.
Komanso uzisambira pawekha, ndipo zipangizo zamsambo uzibisa pamalo
pobisika. Nthawiyi imaoneka pa mwezi kamodzi. Ndiye osathira mchere
mum’phika ngati waphika ndiwo pamene amayi ako achokapo, uzituma mmodzi
mwa anyamata kuti adzakuthirire mcherewo mum’phikamo.’
35
Nyumba zakale zidali zandendera tsopano pakati panyumbayo amaika mnzati
wochirikiza nyumbayo, komanso amakumba kadzenje kuti azisonkhapo moto
wophikira. Kadzenjeka dzina lake ‘dziko’, ndiye mbali zinazo kudzanja lamanja
limatchedwa ‘thala lalikulu’ ndipo lakumanzere ‘thala laling’ono.’ Mbali imene
mayi amakhalako pophika nthawi itakwana yogona onse awiri, mwamuna ndi
mkazi wake, amagona thala lalikulu.
Patapita masiku angapo limakhalapo tsiku lokawonetsa namwali kwa makolo ake
(kuombetsa m’manja). Atayandikira kunyumba, phungu pamodzi ndi namwali uja
ndi ena operekeza amaomba m’manja mumvekere, puuu!Puuu! Puuu! Atafika,
amalandiridwa ndi makolo anamwali uja. Ndiye imeneyo ndiyo nthawi yoti
makolo apereke malangizo awo monga motere:
‘Tiyankhulenji, ndalama yanga ndi iyi. Lero mwakula musadzachitenso utchisi
(uve, kapena kukana kutumidwa), musamapisanso mum’phika ayi. Muzindidikira
mpaka n’tabwera, chifukwa mudzachita masaya ndipo pakamwa padzakhala ngati
pakamwa pa nsupa. Tikakuyitanani, muzigwadanso.’
Mjere
36
Mjere
Chimkoko
Nyawuyi maonekedwe ake ndi olingana ndi makala. Chimenechi amasaka ndi eni
mudzi, ndichonso chimayambirira kuvina. Tsono ng’oma zili m’bwalo amayi
atadzanso moyandikira bwalolo mwadzidzidzi amangoona kumbuyo kwawo
chilombo chawazingira ndipo amasowa kothawira.
Chinamwali chopinda
37
Chisamba
Chamba chimenechi ndi cha amayi okha okha. Tsiku limene pamudzipo wina
wamwalira ndipo ngati pakhale gule wamkulu namkungwi amapita kumidzi
yozungulira kukamema anamkungwi anzake, kuwadziwitsa za chisamba
chodzachitika usiku wa tsikulo. Chidziwitso chake amapereka thonje ngati kalata
yachidziwitso. Madzulo amayi onse amasonkhana ndipo onse amalowa msiwamo,
n’kuyamba kuvina mozungulira mtembo uja. Dzina lake amati kulonjera maliro
ndipo ololedwa ndi okhaokhawo amene adameta, osameta amatulutsidwa.
Amavina kanthawi kenaka n’kuleka napumulira. Akatha kudya chakudya
amayambiranso kuvina usiku wonse. Pamene chisamba chilli m’kati, gule
wamkulu amakhala m’mbalimo nachezera. Gule wake ndi monga Kasinja ndi
Kapoli.
38
iye amaitanidwa n’kumavinira limodzi ndi amayiwo ndiponso n’kuchezera limodzi
ndi amayiwo.
Tsonotu zikatero mavuto amakhala pa phungu uja. Ndiye phungu uja amayenera
kumvetsa zonsezi ndipo kutacha amamuitanira pambali naonjezanso malangizo
aja. Kenaka amamuchenjeza kuti ayenera kukwaniritsa malangizo onse aja. Koma
akakhala mwana womvera, waulemu, wotumika, ndi wosapisa mum’phika, makolo
aja amangoti, “Tilibe mawu ambiri, pitirizani makhalidwe omwe aja. Chifukwa
kalitengera adaoletsa mazira ampheta.” Zikatere phungu zimamukondweretsa
kwambiri.
39
Alipo ena apuludzu amene sapita nawo ku maliro oterewa amangopenya
mosaganiza kuti tsiku lina iyenso adzafa. Tsono chakudza sichiimba ng’oma,
mosayembekezeka mwina maliro amamuonekera iyeyo. Uthenga utafika kwa
mfumu onse amauzidwa nasonkhana pasiwapo. Akakhudza, mfumu imalamula
kuti anyamata apite kuthengo(kumanda), tsono opita kuthengo amati, “Ife njira
yakumanda sitikuiona atilozere ndi iyeyu.” Izi zitanthauza kuti iyeyo sapita
m’maliro, umenewu umakhala mlandu. Mwina amatchera pokaika maliro ndipo
amati adzafotsere yekha.
Dambule
Chaka chilichonse pamakhala mwambo wolambula manda. Wakunjira amauzidwa
ndi mfumu kuti tsiku lakutilakuti tidzalambure manda. Amayi onse amakonzekera
ziphiko zodzadya patsikulo. Litakwana tsikulo onse amasonkhana kudambuleko,
komatu tsikulo lisanafike wakunjira amasamutsa zilombo zonse nakaziika kwina.
Amalambula kwakuti moto usadzalowemo. Ana osameta ndiponso atsikana
osakwatiwa ndi kumetedwa saloledwa kulambula nawo.
40
Pali chikhulupiriro chakuti munthu akafa amauka chinthu china monga fisi,
kambuku, insa, mkango, mvuwu ndi zina. Makolo adakhulupirira kuti Chauta,
Mphambe, Chisumphi, Leza sapha munthu koma mfiti ndiyo imachita izi.
Chifukwa cha chimenechi pamatenda ndi pamaliro amagwirana ufiti. Palinso
chikhulupiriro chakuti mzimu wamunthu wakufa umabwereranso kumudzi
n’kumacheza ndi anthu amoyo powalotetsa maloto.
Tsiku lakutha msinkhu namwali, amayi amasonkhana nakhala naye masiku atatu.
Panthawiyi iye saloledwa kutuluka, koma nthawi yausiku yokha. Ngati namwaliyo
anali wosakwatiwa, makolo ake amafuna munthu womakakhala ngati mwamuna
wake masiku ena. Munthu wotere amatchedwa ‘fisi’ popeza amafika nthawi
yausiku yokha ndipo anthu ambiri samadziwa. Iye amachoka usiku kapena
kum’bandakucha. Makolo a namwaliyo amapita kwa mfumu ndi nkhuku nati,
“Mwana uja wakula.” Amatero kuti mfumuyo ipatukane ndi mkazi wake kuopa
kuti angadule namwaliyo, ndiponso kuti mfumu ifune mankhwala oti namwaliyo
azadye. Chinanso ndi chakuti ngati mfumu ili ndi mzinda izikhala itadziwa kuti,
chaka chino ndimeta namwali pabwalo langali. Itafika nthawi yometa, namwaliyo,
ankhoswe akuchikazi amapita kwa ankhoswe akuchimuna nawauza za chinamwali.
Mwamsanga akuchimuna amasonkhetsa chuma, mbuzi, nkhuku, mphasa ndi zina
zoyenera pa chinamwali. Izi zonse zimaperekedwa kwa mfumu. Dzina lake la
chumachi amati, ‘mtulangala’, ndipo mfumuyo imagawana chumacho ndi
amalume ndi makolo ake a namwaliyo.
41
mtengowo ‘Mtengo wa namwali’ namavina chisamba ndi namwaliyo. Kumtengo
wa namwali kumakhala malango ndi mavinidwe ake. Panthawi yamadzulo amafika
amuna kudzavina mnjedza ndipo amayi amafikanso kubwaloko ndi namwali
atangomveka thewera ngati mbusa (mnyamata wolisha ng’ombe), mawere ndi
matako akuonekera.
Panthawiyi amayi amafika ndi namwali pakhomo lake naimba nyimbo nati,
“Tayalani maye. Tayalani maye, tayalani maye, tayalani mphasazo, namwali
agonepo.” Mwamsanga namwali wamwamunayo amayala mphasa ndipo namwali
wamkaziyo amagonapo. Amayi amaimba ng’oma ndi nyimbo zawo pamphepo,
ndipo namwali wamwamunayo amawafupa. Patsiku loshambula mowa kapena titi
kuviirira zimafika nyawu zovina masana. Mayina awo ndi awa: Chabwerachaona,
Kachipapa, Kavinsabwe, Njovu ndi Jere.
Kavinidwe
M’njovu amalowamo ndi ankhoswe akuchikazi awiri ndi akuchimuna awirinso
atasenza chimtengo.
Potsiriza mfumu imapereka mbuzi ndi mphasa kwa Njovuyo ndiponso chikatiko
(mbiya) chamowa. Atatha izi amameta, ndipo pamakhala tsiku lokavinira namwali
wamwamuna. Atatero anamwaliwo amaloledwa kugona pamodzi.
42
• Mwamuna akakhala kubwalo kwa anzake, ndipo ngati iwe waphika
chakudya uzituluka pabwalo ndi kutsokomola kuti mwamunayo adziwe.
Koma ngati mwamuna sadziwa ichi, ali ndi mlandu.
• Mphotho zonse za pachinamwali zimene zimapatsidwa kwa mkaziyo ndi za
phungu wake wa namwaliyo.
• Mkazi kapena mwamuna akachita chigololo amadula mnzake.
• Tsiku lovinira mwamuna amavina chomuzungulira namamuimbitsa; ngati
alakwa ndiye kuti chakanika chinamwalicho.
• Ntchembere ziwiri zimati mwamuna akachoka mkazi osamameta tsitsi,
ndipo ngati ameta amatsimikiza kuti amachita chigololo. Ndi
chimodzimodzinso mwamuna akameta tsitsi mkazi akachokapo.
• Nthawi zonse pogona namwali amaimba nyimbo yolaula, ndipo ngati
mwamunayo imulaka, apo chinamwali chamulakanso.
• Tsiku loyamba kulowa panyumba amapha nkhuku yophikira kumodzi ndi
mankhwala. Poika mankhwalawo mum’phika mwamuna ndi mkazi
amagwirizana akuimba nyimbo.
• Ana saloledwa kudya nawo nkhukuyo koma eni okhawo.
• Ngati mkaziyo akudwala matenda achikazi sayenera kuphika madzi osamba
mwamuna.
43
kuti namwali akudwala.” Mfumuyo mwachisoni imangokhala chete podziwa kuti
anthu aziganiza kuti ndiye wapha namwali koma chikhalirecho si choncho.
Akatsuka maliro ndi kudzoza mafuta, anthu onse amalira. Amuna amasonkhanitsa
makasu napita kukayamba kukumba manda. Akazi amasinja mphale kuti aphike
nsima ya amuna ogwira ntchito kumanda. Mandawo amakumba kwambiri.
Atamaliza zonse amapita kumudzi kukanyamula mtembo. Amaikanso pamodzi
miphika, nsengwa, mithiko, zipande, ndi zina zonse, monga mwa katundu
wachikazi, zomwe ankagwiritsa ntchito.
Mkazi wachitengwa
44
mnyamatayo kuti chitengwa chakanika. Panthawiyi mnyamata samakhala
wosangalala pokumbukira mavuto amene iye amawaona.
Pokanena, mwina amaima panjira naitana dzina la mlongo wake wa mkaziyo nati,
“Mlongo wanu wamwalira pamudzi wakuti!” Amatero poopa kumenyedwa ndi
anthu apamudzipo. Akumvawo amapangana nati, “Tisakhale tiyeni, ukakhala
mlandu tikakamba komweko.”
Pofika kufupi ndi mudzi amaima kunjira namalira. Eni mudziwo amapita ndi
mbuzi yoti anthuwo alowe m’mudzimo. Akalandira amalowa m’mudzi
mwankhondo, koti atha kumenya munthu.
Ndipo akunjirawo amati, “Chabwino tipatseni mbuzi yotidziwitsa kuti wathu ali
pano.” Ndipo amapatsidwa. Akatero amati, “Chabwino, tsopano tipatseni mbuzi
ina yakuti maliro atuluke.” Mwamsanga amafuna mbuziyo nawapatsa, nadulanso
mkanda wovomerera mlandu. Maliro otere mwina amanyamulidwa ndi eni napita
45
nawo kwawo. Akaika maliro amabweranso patsiku lometa kumudzi kumene
mkaziyo adamwalilira.
Akafika amati, “Tafika kudzatsiriza nkhani yathu ija.” Eni mudziwo amati, “Izo
nzoona popeza uwu ndi mwambo wakale.” Aja amasonkhanitsa chuma
nachipereka kwa eni maliro. Koma ngati chasowa amayesa kudandaula kuti,
“Pepani mutikhululukire kwinaku popeza tayesetsa uku ndi uku, koma sitidapeze
chuma chokwanira.
Ndipo eni maliro amati, “Kodi mumachiyesa chapafupi kutenga mwana wa eni
n’kubwera naye pamudzi wanu; sikuba kumeneku, kodi? Ngati mutipatsa chuma
chosakwanira ife sitilandira.” Apamudzipo amayesanso kubwereka chuma kwa eni
omwe ali nacho, napereka chikapezeka chokwanira.
46
Pamaukwati nthawi zonse pamakhala ankhoswe oyang’anira zovuta za mabanja.
Amayi ndiwo amadziwa kwambiri maonekedwe ndi mayendedwe a anamwali.
Ndiko kunena kuti pamene namwali ameta, monga tanena kale, amayiwo
amaonetsetsa banja latsopanolo. Iwo akaona kuti mkaziyo ndi wotopa,
mwamsanga ankhoswe akuchikazi amauza namwaliyo kuti afulule mowa
woonerana ndi ankhoswe akuchimuna. Ataphika mowawo amaitana ankhoswe
akuchimuna, nati, “Bwerani kuno kuli mowa wachinkhoswe.” Atafika aja
amawadziwitsa kuti wanuyu adalasa, kutanthauza kuti mkazi wake ali ndi pakati.
Mosavutika ndi kuyankha akuchimuna amavomera.
Atafika uko amalira nakakhala kumene amuna a pamudzipo ali. Uko amawapatsa
moni, nawafunsa kuti, “Mwamva zoipa?” Ajawo amati, “Eya!” Eni mudzi amati,
“Monga tidakuuzani kuti wanu adalasa, koma lero nyama yolasidwayo yafadi.”
Akunjira amati, “Inde, izo zamveka koma wangolakwa ndi Chauta.” Eni mudzi
amati, “Tipatseni mkanda wovomera mlanduwu.” Ndipo akunjirawo amapereka
mkandawo. Ankhoswe akuchikazi amauza anyamata a pamudzipo kusonkhanitsa
makasu ndi kupita kumanda. Akukumba mandawo ankhoswe aja amakamba
nkhaniyo. Ndipo amapereka chotulutsira maliro, chomwe chikhala mbuzi imodzi.
Amapita kumanda mwaliwiro. Maliro otere madoda ndi amayi apakati amalira
mowafulatira monga mwa miyambo ya Achewa.
47
(khweru) ndipo amuna omwazikawo amadziwa kuti wakufayo watumbulidwa
ndithu. Tsono anthu amafika nayamba kukwirira malirowo. Atatha amapita
kumadzi kukasamba ziwanda; pobwera kumudziko amawaulanso makasu.
Amagona pakhonde masiku ena natuluka patsiku lometa.
Munthu wakhate
Nthenda yakhate idadziwikanso kalekale pakati pa Achewa ndi kuopsa kwake.
Koma makhwala ndi malewedwe ake sadadziwike. Nthendayi imafala
mumphweya timapuma. Imafalikira anthu amene alipafupi ndi odwalayo monga
ana, mwina n’chifukwa amanenera kuti ndi nthenda ya pamtundu. Ndipo nthendayi
imakhala nthawi yaitali isanayambe kuonetsa zizindikiro.
Koma ngati wodwala nthendayo ali ndi banja lake, banjalo limakhala naye
pamodzi ngakhalenso ana ake omwe.
Anthu odwala nthendayi amakhala nthawi osafa msanga, koma ziwalo zina
zimaduka monga zala, mapazi, ndi zina. Zikatero munthuyo amakhala wozunzika
ndiponso wosalimva kukoma dziko lino lapansi. Ichi chimaipira anansi ake nati,
“Akadayenera kufa msanga ndithu.” Ndipo chifukwa chosafa msanga apo amatcha
nthendayi dzina lakuti, ‘Nthenda yalizunzo’.
48
ndi chisoni chokha komanso chimwemwe podziwa kuti munthu azunzika nthawi
yaitali. Pokumba manda amangokumba pang’ono, ndipo atamaliza amachoka onse.
Anansi a wakufayo amamutenga namukulunga mumtolo waudzu. Maikidwe ake
m’mandamo amangoponya ngati galu koma osakwirira konse.
Manda ake Sali pamodzi ndi ena koma kwina kutali. Manda otere alipo lero lino
m’midzi yambiri, ndipo anthu amachita kupitapo. Pamaliro otere padalibe kumeta,
koma amangowamba ziwanda nawaulanso makasu awo, kupha mizimu.
Nthendayi idadziwika kale lomwe pakati pa Achewa, ndipo idali yoopsa monga
nthenda yakhate ija. Matengedwe ndi machiritsidwe ake sankadziwikanso.
Nthendayi ikayamba m’banja, mayi kapena mmodzi mwa ana a m’banjamo
kapenanso banja lonselo limatulutsidwa m’mudzimo kukakhala kunja kwa mudzi
kutali ndithu monga mtunda umodzi kapena iwiri.
Nthendayi ikagwira mwana wa mbanja ndipo pomusamalira bambo ndi mayi ndi
ana ena amagona naye pamodzi. Nthawiyi kuti ntchentche zili ngw’a, ngw’a,
ngw’a, iwo amangozisiya osazisamala konse, ngakhale zili kukhala m’maso
kapena pathupi koma osazipitikitsa.
Njira yopita kumeneko imatsekedwa kuti anthu ena opita paulendo angadzere njira
yomweyo. Amasamalitsa koposa, ndipo kutero kudali kwabwino popeza ngakhale
lero zikuchitikabe monga m’maiko olongosoka. Amatero poopa kufalitsa
nthendayo. Patsiku lomwalira wodwala mmodzi wa m’banjamo amachoka
nakanena kumudzi kuti wakuti wamwalira. Ambiri samafika kumaliroko koma
achinansi owerengeka okha. Enawo amangolirira kumudzi osapita konse
kumaliloko.
49
Pamaliro otere satumiza anyamata okanena kumidzi ina, chifukwa a midzi
yozungulira samabwera kumaliroko. Mwambo wa Achewa pamanda
amakhazikapo nkhadze womwe ndi mutu wamitengo yopanda masamba womwe
umakhala ndi tinthambi tambirimbiri ndipo masamba ake ndi tinthambi tomweto.
Uzimba
Uzimba ndi chinthu chodziwika m’dziko muno ngakhalenso pakati pa mitundu ina
ya dziko lapansi. Nyama zomwe zimapezeka m’tchire ndi mvuwu, ng’oma,
ntchefu, insa, mphoyo, mkango, nguluwe, kaphulika, mbidzi, nswala, mphalapala,
m’mbulu, kambuku, fisi, chuzu, nkhwere, kalulu, chiuli, kanungu, nungu, nengo,
chiuzimbi ndi kamundi.
Ndipo angakhale machitidwe ake ndi zipangizo zake zimasiyana, koma cholinga
chake ndi chofuna nyama kutsuka m’kamwa m’mene nkhuli idaonongamo.
Amachita izi m’midzi yonse imene iye watumidwa kukanena zauzimba. Pochoka
apo amati, ‘Ndithu nyama nayi,’ nayesera kudya chimangacho ku magazi a nyama.
50
Kumemeza liwamba kumakumbutsa kuti m’mabanja onse kumene liwamba
lamemezedwa alongosole liwamba pakupatukana m’nyumba. Izi zikusonyeza kuti
usiku woti mawa kuli liwamba mwamuna ndi mkazi m’banja lililonse samagonera
pamodzi, kuopera kudula liwambalo kuti angaononge mpingu (tsoka).
Popita kuuzimbako mwini uzimbayo amatenga udzu umene iye anangonapo usiku
uja. M’njiramo iye amafuula nati, “Liwambalo! Liwambalo! Wihi! Liwambalo!
Liwambalo! Wihi!”
Ali pamalopo amagona paudzu uja ndipo atafika onse amampeza ali mtulo.
Kugonako kusonyeza kuti nyama zigonenso. Atadzuka amalonjera onse nati,
“Mwabwera nonse?” Iwo amavomera nati, “Eya.” Ndipo amayamba kunena
malamulo auzimba nati, “Muuzimba mukaona insa (gwape), kalulu, nkhanga,
mbawala, ngoma, ndi ntchefu, izo zonse muphe; koma mukaona nyalugwe, njoka,
fisi, mkango ndi nkhandwe; muzithawe popeza si ndizo ndifuna kuti muphe ayi.”
51
Akafika kumudzi amuna onse amakumana pabwalo. Ndiye miyendo yonse imene
idakadzulidwa amaiunjika pabwalopo n’kumagawana molingana. Pogawanapo
sipamakhala wodandaula konse.
Uzimba uli pawiri, wina amatentha tchire la munthu wina wake ndipo ngati
munthu wina alumidwa kapena kulasidwa, pamenepo mlandu wake amalipa
tchirelo. Uzimba wina ndiwo wongopita m’matchire ambiri a anthu ena amene iwo
adatentha kale. Mlandu wa anthu olumidwa m’matchire a uzimbawo amalipidwa
chuma chambiri, makamaka mbuzi zambiri popeza Achewa adali ndi mbuzi
zokhazokha ng’ombe zisanafike.
Malamulo a uzimba
• Tsiku lomemezedwa liwamba sikuloledwa mwamuna ndi mkazi wake
kugona malo amodzi kuti kungakaoneke ngozi ku uzimbako.
• Pomemeza liwamba amatenga chimanga chofiira kufanizira magazi a
nyama.
• Mwini liwamba amagona paudzu kapena pamasamba. Amachita izi
chifukwa masiku onse amasendera nyama paudzu kapenanso pamasamba.
• Mwini uzimba amagona pamalo ponyamukira liwamba kuti nyamanso
zigone.
• Amene ali ndi mkazi wapakati saloledwa kupita nawo kuuzimba kuti
kungakaoneke mpingu.
52
• Anthu akalasana kuuzimba, mwini wa uzimba amapereka nkhuku popeza
ndi iye adamema uzimbawo.
• Akazi saloledwa kupita nawo kuuzimba.
• Nyama zophedwa kuuzimba mwini uzimba amapatsidwa mwendo wathako
wa nyama iliyonse yophedwa.
• Mkazi mwina mwana wamkazi wa mwini uzimba saloledwa kutuluka
m’nyumba mpaka auzimba atabwera; amatero kuti nyama zingathawe
kuuzimbako.
• Mwini uzimba atalandira miyendo, imagawidwa kwa mfumu ya mudzi
popeza nayenso imalongosola nawo liwamba.
Uzimba
Kapolo
53
yoopsa. Amapatsidwa chakudya chosakwanira ndipo nthawi zina amadwaladwala.
Kapolo akakhalitsa amatchedwa ‘mwana’ ndipo dzina la ukapolo silimamvekanso.
Ukapolo wina udali wogulitsidwa. Pali mitundu ine imene imapeza chuma chawo
pogula ndi kugulitsa akapolo. Ndiye wogulitsidwa amakhala mwana wosamvera
(puludzu). Makolo ake akatopa naye amangoti, “Tengani uyu. Bola mutipatse
thumba lamchere kapena malipande awiri ansalu ya biriwita (nsalu yakuda).”
Ukapolo wina udali woti ukakumana naye munthu amene utam’dziwiratu kuti
sangalimbelimbe, otereyo umam’bweza kumene walunjika (kumsemphetsa
chikuwa). Zitatero umamusandutsa kapolo namakugwirira ntchito. Ngati ndi mkazi
kutsogolo amasanduka mkazi wako n’kumanga naye banja, zikatero ukapolo
umathera pomwepo.
Kapolo wotero poyenda amamuthira ufa m’khutu kapena m’kamwa kuti asathe
kumva, kufuula ngakhalenso kulira. Ukapolo wina umabwera chifukwa chakuti
mwina mlandu ukakula ndipo dipo lake lasowa, ndiye amangopereka munthu
kusandutsa dipo la mlanduwo. Zikatero samatchedwa kapolo, amakhala ngati
chiweto ndipo amakhala movutika.
Nthawi zina munthu amadziyendera, ndiye akakumana ndi anthu omenya nkhondo
amamgwira n’kutsogoza kum’pititsa kowirira namukhazikitsa pansi. Kumeneko
amamuthira ufa wa lipoko m’kamwa n’cholinga chakuti asathe kuyankhula
kapenanso kukuwira ena. Kutada amayenda naye mozungulira. Mwina
kukam’fikitsa kutali kwambiri, n’kubwerera nayenso kupita naye uku ndi uko
ndipo kukamacha amapita naye kunyumba kwawo atatopa kwambiri.
54
Ukapolo wamkazi sumachedwa kutha maka ngati ndi wokongola, chifukwa mfulu
zimamukwatira ndiye ukapolowo umathera pomwepo. Mwamwayi mwina
amakwatiwa ndi mfumu kumene.
Pali nthano yochitsa chidwi imene ikuti azungu a mishoni oyamba monga Rev AC
Murray ndi Rev Robert Volk mu 1888 adapempha mfumu ya Agoni, mfumu
Chiwere, kuti awapasire ana oti awaphunzintse, koma mfumuyo idapereka ana a
akapolo kwa a mishoni. A kapolo aja adaphunzitsidwadi, ena nasanduka
aphunzitsi, ena akapitawo mpaka kusanduka abusa a Mawu a Mulungu.
Kopolo wogulidwa
55
mnyamatayo amakhala wosasangalala nthawi zonse pokumbukira makolo ake
ndiponso ntchito ndi masungidwe ake kwa mbuye wake.
Maliro akapolo sadali monga momwe adali mwana wa mfulu. Anthu amapita
kumanda nakumba pang’ono, natenga malirowo ali okulungidwa m’tchika
labango. Kukakhala kuti mbuye wake wa kapoloyo adali wabwino, amachita zonse
monga momwe anagachitire ndi mwana wake.
Lero dziko lonse la Africa ndi mayiko ena omwe, ukapolo udaletsedwa ndi Boma.
Pamene Dr. David Livingstone adayendera dziko lathu lino adamva chisoni
kwambiri ndi anthu amene amvutiak kamba kamalondawa. Ndipo chifukwa cha
ntchito yake yotamandika malondawa adaletsedwa ndi maboma ambiri.
Ukapolo
Padali ana omwe adali apuluzu ndi osamvera ndiponso omva zawokha. Oterewa
kukadza amalonda, maka aluya amawagulitsa ndi mchere mwina litaka la nsalu.
Ogulitsidwa uja samadziwa kuti wagulitsidwa. Amalonda aja akamanyamuka,
wogulitsidwa uja amauzidwa kuti awaperekeze alendowo kuti awatule kunjira.
Ndiye akamafuna kubwerera amamuumiriza kupitiriza ulendo. Ngati avutitsa
amamumenya kolapitsa ndipo ulendo umakhala womwewo wopitiratu.
56
n’kumenya pamwamba pa muundawo n’kuitana dzina la malemuyo. Nthawi
yomweyo malemuyo amatuluka yekha m’mandamo. Zikatero amamuphanso
nasenda thupi lonse n’kuyamba kugawana ziwalo molingana. Zikatero
amamwazikana. Pophika amaika malo obisika omwe ena amati pansi. Itapsa
amadya mobisa kwambiri. Mwamuna ndi mkazi onse akakhala mfiti ati kudya
kwake sikuvuta konse.
Ufiti ulipo ungapo, wodya anthu ndi wampheradumbo. Mfiti zina zimapha munthu
chifukwa cha zimene alinazo monga ziweto, galimoto ndi zina. Izi mfiti sizidya
nyama ya munthu. Mfiti zotere tikhoza kuzitcha mfiti za m’pheradumbo
(m’pheranjiru). Zimangopha ndi mankhwala aululu, mwina ndi mizu kapenanso
zolengedwa zina monga ulembe (sumo). Komanso pali mankhwala ena ongolemba
malire kuti utalumpha mzerewo ungafe ndithu. Mankhwala ena otemberera
potemba amati, “Dzuwa uliona potuluka pokha, polowa sulipenya.”
Pali zitsamba zina zaululu zimene munthu atadya amafa. Pakauka mkangano
pakati pa munthu ndi munthu mnzake, mmodzi mwaiwo amafunafuna mankhwala
ophera mnzakeyo pomudyetsa. Maphedwe ake amathirira kuchakudya monga
nsima, mowa kapena kuphala lachimera, mwinanso ku tiyi.
Mfiti ikadziwika anthu amaiopa ndi kusayifunira zabwino, angakhale achibale ake
omwe.
Kusamalira mtembo
57
Akuthatha ndi imfa, ena amagwira miyendo yonse iwiri n’kuiphatikiza, ena
amagwira manja n’kuwakanikiza mbali imodzi yamutu mokhumatitsa, ena
amatseka maso kuti asang’omboke, ndipo thupi lawakufayo litazizira amatenga
mkuzi n’kunjata manja ndi miyendo; amanjatanso kuchigama mpaka pakati pa
mutu.
Amakauza mfumu ndipo mfumu ija ikabwera imalamula kuti atsuke, ndipo
amamusambitsa thupi lonse n’kumuveka ziwalo zonse osaiwalanso kumudzoza
mafuta. Zonse zitatha mfumu imauzidwa kuti, “Tatsuka.” Ngati ndi mayi,
womutsuka amakhala ntchembere zokhazokha, koma ngati ndi mwamuna otsuka
amakhala ndoda zokhazokha.
Pambuyo pa zonse mfumu imalamulira ndi mawu niti, ‘Tiyeni tikhuze ngoziyi.’
Ndiye woyambirira kukhuza amakhala mfumu, kenaka onse amatsatira pambuyo
pa mfumuyo n’kubuma. Poika chitanda amasanja ndi kuikapo udzu, ndipo
pamwamba pake amaikapo mphasa. Mferekazi (dzinali ndi lamkazi amene
mwamuna wake amwalira) amakhala ndi kansalu m’manja n’kumaingitsa
ntchetche mpaka nthawi yochotsa maliro. Popita kumanda, mferekazi
amamufunditsa nsalu thupi lonse kuyambira kumutu mpaka m’munsi. Pamakhala
amayi omugwirizira, makamaka alamu ake. Atafika padzenje mferekaziyo amatapa
dothi lodzala chikhato n’kuthira m’mandamo. Kumeneko amati n’kulawirana
ndiponso kuuza mzimu wa wakufayo kuti usakamukumbukirenso.
Asing’anga
Pali asing’anga ochiza anthu odwala. Tsono ena zizimba zake amazipeza potenga
ziwalo za munthu. Asing’anga ena amatha kuthandiza munthu wosabereka,
mwamuna kapena mkazi omwe amatchedwa chumba. Sing’anga akhoza kukhala
mwamuna kapena mkazi. Ziwiya zosungiramo mankhwala ndi mphondo za
ng’ombe, nkhosa, nyanga za nyama zakuthengo monga insa (gwape), chipembere,
ngoma ndi zina.
58
achinansi a wodwalayo nati, “Kodi amaneyu timuchitenji?” Yankho limati,
“Iphani, mwina mulumazeni kapena mudooleni maso.” Mfumu ikafunsidwa
funsolo kuyankha kwake kumakhala kwakuti, “Ingophani, pano kuti anthu akhale,
chifukwa mudzi kapena dziko ndi anthu, ndipo thengo m’mabala.”
Mtsiriko
Kutsirika kwake kudali kwakuti ukaba ugona pomwe wabapo mpaka kukuchera
pomwepo. Ngati waba nkhuku, nkhukuyo imalira m’phikamo mwina m’mimba.
Mtsiriko wina udali woumitsa mimba, wina pakamwa kupotoka. Munthu wofuna
kuba ziweto amangopeza khola lili pakati pa nyanja. Nyumba ikakhala yotsirika
mwina mfiti siingathe kuiona. Akakhala makhola aziweto mwina amazingidwa ndi
zilombo monga mikango. Munthu atayandikira zilombozo zimamupitikitsa.
Mankhwala
Pofunsira mbeta pamafunika mankhwala. Pofuna ntchito pamafunika mankhwala
opezera ntchito. Pofuna kukwezedwa patchito pamafunikanso mankhwala. Amayi
apamitala amafuna mankhwala otchedwa ‘konda ine’. Mankhwalawa amathiridwa
ku ndiwo mwina mumkhate wosambiramo. Mwamuna wosakhazikika pakhomo
kapena woyendayenda amamudyetsa mchira wabuluzi chifukwa buluzi
sachokachoka, mwake ndi m’khonde.
Matsenga (masenga)
• Munthu wolemera amakhala ndi mantha podziwa kuti atha kulodzedwa ndi
mfiti mwinaso kufa msanga.
59
• Mkazi wankhope yokongola sayenera kukana amuna podziwa kuti ngati
atero atembereredwa ndi amasenga.
• Amuna a nyawu, amauza ana kuti, “Ngati muulula nyawu potsiriza pake
mudzachita misala.”
• Amakhulupirira kuti munthu atangolemba panjira nati, “Ngati uje aponde
pano adzachita misala, kupunduka kapena kumwalira wosadwala konse.”
Ambiri amayenda moopa posadziwa chimene mdani waika panjira.
• Pamakhalanso wina amene amadziwa mankhwala ochiza matsengawo,
ndipo amati, “Ngati munthu amene adalodza iwe sadya nsima kapena sagona
monga anthu onse, matenda amenewa satha konse. Koma ngati ndi munthu,
matendawa atha.”
• Anyawu amaopsa anthu nati, “Ngati ubisala pathengo kuti uone nyawu
zathu, maso ako achita khungu.”
Lero tili okondwa kuti anthu ena ayamba kuzindikira kuti ufiti ndi matsenga ndi
zachabe.
Masasa
Moto ukayaka amausonkha ndi nkhuni zouma kotero mudzi wonse umapala moto
pamenepo. Malamulo amati munthu asaunike kapena kulowa ndi moto
m’mudzimo, popeza kutero kudali kuunika mudzi. Zikatero umakhala mlandu.
60
Nthawi zina pamasasapo mavuto osiyanasiyana monga mikangano ndi ndewu.
Akuluakulu amayesetsa kuweruza milanduyi mwachilungamo. Mwachitsanzo
nkhuku ya munthu wina ikasowa, munthuyo mwina angokayikira mnzake amapita
kukamwa mowa dala. Akabwerako amakuwa nati, “Mverani! Nkhuku yanga
mwadya, ndikupitirani kwa sing’anga kotero zimene muone pano ndi zimenezo.”
Kutacha nduna za mfumu zimalawirira kukhomo kwa wotukwana uja ndi
kumufunsa kuti, “Kodi kutukwana kuja mudayambana ndi yani?” Woyankha
amati, “Inetu ndimalira nkhuku yanga imene munthu adandibera dzulo masana.”
Funso limati, “Kodi munthu amene wakuberaniyo mwamugwira?” Yankho: “Ayi,
sindinamugwire.” Ndiye chiweruzo chimati, “Popeza wakubayo simunamgwire
ndiye mwatukwana mudzi, kotero mulipira mkota wa mbuzi.”
Munthu wogwidwa ndi nkhani zachiwerewere dipo lake lidali kuphedwa onse
awiri. Izi amachitira popewa kuti zilombo zisamalowe pa msasapo
n’kumadzagwira ziweto.
Mankhwala ena adali temberero. Anthu awiri akamenyana, koma winayo poona
kuti iye wamenyedwa kwambiri ndiye amayamba kunena zambiri mosalingalira,
nati, “Iwe, ine sundidziwa kuti ndine swiswiri sapita m’chimera, ndipo lamawa
suliona potuluka.” Winanso amati, “Inenso ndine mwana wa Pite, bololo sakonda
madzi, ndipo lamawa uliona potuluka pokha koma kumene lizilowera suliona.”
Anthu oonera ndewuyo amamvetsetsa zonsezi nazisunga. Mwatsoka winayo
amadwala ndipo abale ake amapita kwa mnzake wotemberera uja nati, “Monga
mwa mawu anu aja mnzanuyo akudwala.” Koma iye amati, “Koma ine dzulo lija
ndidangonena mosaganiza bwino.” Koma enawo amati, “Ayi mudanenetsa bambo,
kapena mayi. Nanga wathuyu adwala bwanji?”
Patsiku lomwalira munthuyo, achibale ake amati, “Mnzanu uja wamwalira monga
mwa mawu anu aja.” Munthuyo nkhawa ndi mantha, amayesa kukana, koma
sizimveka konse. Iye amalipitsidwa chogonekera maliro, ndiponso dipo lenileni.
Kuyambira tsiku limeneli, munthuyo amadziwika kuti ndi mfiti ndipo anthu
amachita naye mantha nthawi zonse.
61
Maliro a munthu womwa mwavi
Mwavi ndi dzina la mtengo waululu wakupha munthu. Koma anthu ambiri
ankakhulupirira kuti ndi makhwala olondola ndipo amangopha mfiti zokha, kapena
wakhalidwe loipa monga chiwerewere.
Mfumu m’mudzi ikaona kuti anthu akutha kufa amaganiza kuti pamudzipo pali
mfiti imene ikutha anthu. Pakati pa Achewa ndi mitundu ina amalingalira kuti,
munthu aliyense yemwe wamwalira idamuloza mfiti basi. Salingaliranso kuti
matenda ena munthu amadzitengera yekha nafa nawo. Atasinkhasinkha mfumuyo
imati, “Kudakakhala bwino ngati ndikatenge mwavi kuti onse adzamwe.”
Mfumuyo imaneneratu kuti, “Pokhala pathu ndi iwe, tikakhale mopenyana ndipo
ndikakaimirira chala changa chakumwendo ameneyo ukam’mwetse mwavi
wopanda mphamvu koma ndikakagwetsa chalacho kwa woteroyo ukam’mwetse
wamphamvu.”
Atafika kumudziko amaitana nduna yake ndi madoda a m’mudzimo nawauza kuti,
“Ndakatenga thumba (mwavi) kuti tonse tiyere, popeza anthu afa ambiri. Onsewo
amavomera mwachimwemwe podziwa kuti mwavi umalondola mfiti, koma wina
amene sali mfiti sumulondola ayi.
62
“Ifani chafufumimba mungandiphere thumba.” Ndipo munthuyo amamwalira.
Onsewo amasekerera kuti munthuyo adalidi mfiti.
Anthu osauka ndi olemera amapezeka pakati pa anthu am’maiko onse. Nthawi
zonse wosauka amagwira ntchito kwa munthu wolemera. Wachuma sasowa
abwenzi ocheza nawo popeza munthu amadziwa kuti ndikakafika pakhomopo
ndikadya zabwino ndiponso ndikagona pabwino.
Komanso pali mawu akuti, ‘Wosauka ndiye amakhala nthawi wosafa msanga
koma wolemera amafa msanga.’
Pakati pa Achewa wina akapeza mbewu kubzala bwino kumunda, ndipo walonga
nkhokwe zitatu, kapena zinayi amayesa tsoka nati, “Ine ndalaulidwa,” Mwinanso
amakhala ndi ziweto zambiri, koma munthuyu sagona bwino masiku onse popeza
amakhala ndi nkhawa yakuti iye munthu wina adzamulodza ndi kumwalira
asanadyerere chuma chake.
M’mawa kutacha amapita kwa munthu amene amadziwa mankhwala osunga thupi.
Ndipo mwiniyo amati, “Inde mankhwala ndimadziwa koma mtengo wake ndi
mbuzi khumi.” Mwamsanga wolemera amavomera kuti apeze chipulumutso.
Ndipo iye amakhulupiriradi mankhwalawo.
Atagona tsiku lina, amalota atulo munthu ali chilili pakhomo kufulama namalodza.
Kutacha m’mawa amafotokozera mkazi wake ndipo mkaziyo amati, “Pepani
amuna anga, ine mkazi wanu wapamtima ndikuuzani kuti pitaninso kwa
sing’angayo kuti akakupatseni mtsiriko wa nyumbayi kuti mfiti zizidzaona ngati
pali nyanja.” Nthawi zonse mawu a akazi samakanidwa, ndipo mofulumira
63
amapita kwa sing’angayo natenga mankhwala otsirika nyumba kuti mfiti
zisafikenso.
Machitidwe angozi yotere akakhala anthu abwino amangoti ndi ngozi. Koma ngati
makolo amwanayo ndi anthu ovuta amanena kuti mwanayo akasungidwe kwa
makolo a mwana womulasayo mpaka atachira. Koma ngati wovulalayo amwalira,
apo pamakhala milandu yopanda dipo lina koma kulipanso munthu wamoyo.
Dipo lotere ndi lija anthu amati, “Dziko kulipa dziko ndipo khungu kulipa
khungu.” Ndipo mwana wolasa mnzakeyo ndiye amaperekedwa dipo, ndipo a
banja linalo amamulandira ngati mwana wawo weniweni.
Ngozi ina ndi yomwe imachitika anthu awiri akamenyana ndipo winayo nagwa
naferatu. Womenyayo amakhala pa mlandu waukulu kwambiri. Atalipilitsidwa
amaika malirowo, nameta nasekererananso.
64
Imfa yadzidzidzi ndiyo imathetsa anthu nzeru, ndipo anthu onse sazindikira
chimene chaagwera kuti n’chiyani. Izi zikutanthauza kuti munthuyo amamwalira
wosadwala konse.
Machitidwe a imfayi mwina amalingana ndi imfa yangozi. Akazi popita kukatola
nkhuni amapita ambiri. Ndipo mmodzi mwa iwo poti akwere mumtengo athyole
chikunicho, mosayembekezera amagwa naferatu. Imfayi imadodometsa anthu
polingalira kuti mnzawoyo wangofa wosadwala.
Koma mwina mkazi amadzuka m’mawa napita kunkhuni, kumadzi ndi kwina
nabwerako ndipo kenaka nasinja mphale. Atamaliza izi zonse madzulo amaphika
nsima kuti banja lake lidye. Ndipo mayiyo amangozindikira akuti, “Ndagona
pano,” nsima wayisiya ili pamoto. Bamboyo poyesa kumfunsa kuti, “Kodi make
Ntchowa mwachita bwanji?” mwina bamboyo sayankhidwa konse.
Amuna ena amapita kuthengo nakaveka mnzawo masamba m’khosi, m’chiuno ndi
pachifuwa, namveka nsalu kumaso, naboola pawiri kuti azionerapo. Ichi ndi
chinyawu chimene chimatchedwa Kang’wing’wi. Ndipo Kang’wing’wi amafika
kumudzi namavina akazi akuimbira nyimbo. Kang’wing’wi amakhala ndi zibonga
ndipo amatha kupha nkhuku iliyonse ndiponso kumenya munthu ndi zibonga.
Dzina la zibongazo amati, ‘zigelo’.
65
Kang’wing’wi
Panthawiyi amuna amakhala ali kumanda. Ataika malirowo amachita zonse monga
mwa miyambo ya Achewa.
Tsiku loyamba nthendayi siimadziwika, ndipo mwina imam’fikira ali pafupi ndi
moto mwinanso pamadzi. Ndipo makolo ake a munthuyo samulola kuyenda yekha
panthawi ya kukhala ndi kufa kwa mwezi.
66
Imfa ya munthu wodwala nthendayi amachita m’njira zosiyanasiyana. Matendawo
akamubwerera pafupi ndi moto iye amagwera pamotopo. Ndipo ngati palibe anthu
pafupi amangopserera. Pofika anthu amapeza kuti munthuyo watha kale kupsa.
Amaitanizana kudzaona zachisonizo natenga zopsererazo naziunjika pamphasa
nayamba kulira maliro.
Mafedwe a anthu ena odwala nthendayi amachitika pamene apita kukasamba. Ali
pamadzipo nthendayi imamufikira ndipo amakomoka ali m’madzimo. Anzakewo
mwina sazindikira msanga kuti mnzawoyo wakomoka. Atakhalakhala amaona kuti
mnzawoyo satuluka m’madzimo. Ndipo anawo amathamanga napita kumudzi
kukauza makolo ake. Anthu onse amafika nayamba kumira kufuna wakufayo.
Akapezeka amamunyamulira kumtunda namuika pamphasa. Kuchokera uko
amapita naye kumudzi.
Maikidwe ake sasiyana ndi maikidwe a maliro ena onse, ndipo amameta nachita
zonse monga mwa miyambo ya Achewa. Pomalizira penipeni amatulukanso
pamtanda.
Moto ndi chipangizo chabwino cha mabanja onse a dziko lapansi. Komanso zoipa
zake za moto ndi zosasimbika. Achewa amakonda kutentha tchire kuti aphemo
nyama mosavuta. Tchire limakhala ndi mwini amene amamemeza kuti tchirelo
litenthedwe patsiku lakutilakuti. Patsiku lonenedwalo anthu amasamala
kulongosola mwambo wopatukana m’banja pogona monga momwe amachitira
uzimba, monga tawerenga ponena za munthu wolasidwa kuuzimba.
Amauziratu anthu tsikulo lisanafike kuti amene ali ndi kanthu kake m’chiremo,
monga mirimo yosiidwa, akachotse tsikulo lisanafike. Patsiku lonenedwalo
amafika onse kudzatentha tchire. Amakhala mbali ndi mbali namayembekezera
kumene nyamazo zingatulukire kuti aziphe. Mwiniyo amauza mwana wake
woyamba ndi mkazi kuti asatuluke m’nyumbamo mpaka tchirelo litatha kupsa.
Amatero kuti nyamazo zisatulukirenso. Akutentha, nyama zimatuluka m’tchiremo
uku ndi uko kuthawa moto. Anthu okhalirawo amaziletsa nazipha kunja kwa
tchire.
Koma mwina nyama ina imalasidwa ndipo ili pafupi kufa imalowanso m’tchiremo.
Koma wolasayo amalephera kupirira poganiza kuti nyamayo itsirizidwa ndi wina.
67
Ndipo Poona kuti mtima ukumuwawa amalowa patchirepo kuti akatsirize nyama
yolasidwayo. Koma nyamayo mwina imathawirabe kutali.
Nyamayo akaitsiriza, koma kuti abwerere komwe anachoka amaona kuti moto
wagundika kwambiri. Amayesayesa kuthawira uku ndi uko ndi kufuula kwambiri
koma motowo umabwerabe. Pofuna chipulumutso amachipeza mumtengo
nakwera, koma popeza moto umalirima kwambiri, malawi ake amakwera
m’mwamba kwambiri. Munthuyo amapsera momwemo, ndipo amafika anthu
nadzatenga mtembo wake kuti akaike m’manda. Apa pamakhalanso mlandu ndi
mwini tchire nati, “Inu mudatiitanira nkhondo kuti ife tidzapsere m’tchire lanu.”
Choncho mwini tchire amapereka dipo kwa eni munthu wakupsayo. Dipo lake
nthawi zambiri imakhala tchirelo.
Ndipo pofuna kutsata bwino imfa yodziphayi tiyeni tiyese kulondola zitsanzo zina
zimene zimachitika kuti munthuyo adziphe. M’banja mwina mkazi amakhala
wolongolola kwambiri. Mnyamata poyamba kukhala m’banja sadziwa mavuto a
banja ndipo pamene mkazi alongolola iye amakhala ngati kapolo wopanda ufulu
weniweni. Pofunafuna chochita chimasowa nayamba kufuna njira yoti angathe
kuzipulumutsa kumavutowo.
Mosachedwa amapita kwa bambo, kapena amalume ake nati, “Ine ndapeza mavuto
pabanja langa mkazi ndiwolongolola, tsono ndimafuna kuti ndimuleke.” Koma
nthawi zina iwowa amamukakamiza, ngakhale iyeyo mumtima mwake sapeza
bwino. Nthawi zonse amakhala wosasangalala nafunafuna njira yothawira
mavutowo. Atalingaliralingalira mwanjira yausatana iye amapeza kuti kuli bwino
angofa. Mobisa, msanga amakwera mumtengo nadzikoleka m’chingwe pakhosi
nafa.
68
amaona mtembowo uli lende m’mwamba. Mofulumira amafuula nati, “Tengani
mphasazo, munthu uja anadzikweza ali pano!” Anthuwo amatenga mphasa napita
nakanyamula mtembo. Anansi ake a munthu wakufayo amati, “Tiyeni tilondole
chifukwa chake chodziphera.” Motero amaitana mkaziyo namufunsa nati, “Kodi
m’banjamu munali ndewu patsiku lija wasowa mwamunayu?” ndipo mkazi
amanena chidachitika m’banja panthawiyo, koma mwina amayesa kubisa kuti
mlandu ungamuvute. Atabisa motero anansi a munthuyo amaulula kuti,
“Munthuyo patsiku lakutilakuti iye adadza kwathu natiuza zakutizakuti.” Ndipo
zikatero pamakhala mlandu.
Maliro a chitsiru
Uchitsiru wina ndiwo woti chitsirucho chimagwira ntchito bwinobwino ndi kuvala
bwinobwino, koma chimangoseka popanda choseketsa chenicheni. Ngati makolo
amuuza mwambo ndi zina, iye sazimvera konse. Koma ngati ndi mkazi, amuna
safuna kumukwatira podziwa kuti chitsiru sichimva ndi kugwira ntchito
molongosoka. Namwaliyo amakula koma uchitsiru sumamuthera.
Uchitsiru wina ndiwo uja wakuti ‘umunthu’ umasowa, samavala ndiponso ntchito
sagwira konse. Makolo akalandira mwana wotere m’banja, amamulera monga
mwamaleredwe a Achewa. Koma uchitsiruwo umadziwika pamene mwanayo
wakula.
69
umaliseche wake. Anthu amene amakumana naye amangoseka koma iye
osalabadira konse.
Mdulo
Mdulo ndiyo nthenda ija yamapapo, ndipo wodwala amasanza magazi kapena
kutsokomola magazi. Koma makolo athu amati nthendayi ndi mdulo ndipo
matengedwe ake ndi aja ndalongosola m’mitu yoyambayi. Gwero lake amati ngati
makolo salinda mwana pamene iye wapita ku ulendo, mwanayo amatenga
nthendayi. Izi ndizo zimene makolo athu ankakhulupirira.
70
Maliro a mkamwini
Mkamwini kale adali wa zaka zambiri zopitirira 18, koma lero alipo akamwini
azaka 14, ndiponso mkazi wa zaka zocheperapo. Banjalo limachitidwa
mwachibwana ngati zamasewera basi. Kudzakhala bwino ngati ichi chidzakonzeka
m’tsogolo muno.
71
kwa iye. Ichi chidali ngati chikhalidwe chawo cha Achewa kuti iye asayambe
kuonetsa kudya kwambiri.
Maliro a nankungwi
Mfumu ikagula mzinda kuti izimeta anamwali, iyo imafuna namkungwi wake woti
azidzalangiza anamwali a pamudzipo. Mfumu imasankha mwana wa mlongo
wake, wamkazi, kuti akhale mfumukazi wake.
72
Kasiya maliro
Panthawi yomwalira iyeyo, mfumu ndi anthu ake onse amamva chisoni ndipo
amatsuka nabuma. Akukumba manda amuna ena amachita nyawu ina yotchedwa
“Kasiyamaliro”. Nyawuyi imapita kumudzi nikavina. Akazi amakondwera ngati
tsiku laukwati chifukwa cha nyawuyo. Koma ena amamva chisoni kwambiri
podziwa kuti mlangizi wawo wapita. Ataika maliro, madzulo nyawu yotchedwa
Kachipapa, imafika naimba nati, “Wapita namkungwi e-e! Talire bwanji maliro.
Wapita namkungwi e-e. Talire bwanji maliro.” Akaziwo amatsira mavume ake,
ndipo amaimba mwina usiku wonse mpaka kucha. Atatero amapita kwawo.
Patsiku lometa mpalo pamafika Njovu ndi Jere, ndipo mfumu imawaza Njovuyo
mankhwala aja a ‘khundabwi’. Powaza mankhwalawo mkazi wa mfumu
amakhalanso pomwepo.
Itakapuma Njovu, mfumu imatenga mbiya yamowa ndi kupatsa Njovuyo kuti
ikamwe. Patsiku lopita kwawo Njovu, mfumu imayenera kupereka mbuzi. Patsiku
lampalo pamafika zinyawu izi: Simoni, Kachipapa, Chabwera ndi Pedegu ndi
kuvina nthawi yamasana.
Wakunjira
Kunyawu kumakhala atsogoleri ambiri, wina ndi Wakunjira. Uyu ndiye wamkulu
wolamulira gule yense ndi zovuta zina. Pamakhalanso ena, ndiwo atsabwalo; awa
ntchito yawo ndi kubwereka ng’oma zoimbira nyawuzo, kusesa ndi kulambula
pabwalo la nyawu ndipo kuyang’anira zonse zochitika pabwalopo kuti zonse
ziyende molongosoka bwino.
73
Pedegu
Atamva wakunjirayo amapita nazo izi kwa mfumu nati, “Auje afuna kuti tivine
nyawu pamaliro awo aja.” Ndipo mfumu imati, “Chabwino ngati ali ndi mphoto
74
zofuna nyawuzo mutha kuuza ana kuti akamemeze gule pamidzi yozungulira.
Wakunjira amaitana anyamata onse kuwauza kuti, ‘Pamudzi pano padzakhala gule
mawa, ndipo inu anayi pitani mulengeze gule pamidzi yozungulira.” Nauzanso ena
a iwo kuti akayendere gule, ndiko kuti akasende luzi ndi kutema chabzero ndi
udzu, ndiponso kukaona m’midzi mmene muli makoko, m’nkhuti ndi m’madzala.
Atayendera, amapita kukaba gule ndi makoko, amapita pakati pausiku anthu
atagona. M’mamawa wakunjira ndi anyamata amalawirira ku dambwe. Ndipo iye
amaona kuti zonse zilipo; koma ngati alipo yemwe anakana kukaba guleyo, uyu
amapirikitsidwa ku dambweko, ndipo amafikanso ndi nkhuku ngati afunanso.
Nthawi yam’mawayo kumamveka, “Ho! Tate waye! Aliko gule.” Uyu ndiye
Kapoli, nyawu ina. Atamva ichi akazi onse amakondwera kwambiri podziwa kuti
lero tidzaimba nyimbo zathu zoimbira nyawu, usiku.
Kapoli
Kapoliyo amangofuula tsiku lonse kuti anthu opita m’njira yapafupi adziwe kuti
kumeneko kuli nyawu. Kumanga nyawu yonse ndi ntchito yakalavulagaga ndipo
mwina imatha nthawi yaitali, koma chifukwa cha kuchuluka anthu, mwina imatha
masana. Si mudzi umodzi umene umachita nyawu, komanso midzi yozungulira.
75
Maliro ake a wakunjira amaikidwa mwaulemu monga a namkungwi.
Popita kumanda amuna amayesa muyeso wamtembo kuti akalinganize bwino malo
oyenera kukumbidwawo ndipo onse amapita kumanda. Akafika uko ndipo
asanayambe kukumba, amafika wina ali mchenje, mphondo yamankhwala
yopatsidwa ndi mfumu nati, “Mfumu ikuti tilembe pamene tifuna kukumba ndi
mankhwala kuti tisapeze zovuta zina pokumba, monga miyala ndi zina zotere.”
Akachita izi, amayamba kukumba mandawo.
Mdondo
Panthawi yampalo pamafika Mdondo, Jere ndi Kasiyamaliro ndipo akazi amaimba
nyimbo zawo nati, “Nyamayo de! Dede! Aye! Nyama mdondo!” Amaimba
motsirirana mavume. Nyimbo ina amati, “Ana amuna n’chilombo adakatenga
nyama kuthengo. O Dede! Aye! Odede aye!” Mdondo ndiyo nyawu yaitali
yokhala, imakhala ndi anthu asanu ndi anayi kapena khumi m’kati mwake monga
sitima.
Zitapita izi zimafika zina zija zovina masana zomwe ndi Kachipapa, Simoni,
Chabwerakumanda ndi zina. Zitafika zimayamba kupereka kasitomu; kugula
76
bwalo kwa wakunjira uja, ndipo iye ndi mfumu amagawana. M’mawa Mdondo
umavinanso nufupidwa mbuzi ndi mphasa.
Ufumu wa Achewa
77
Mfumu itafa, panthawi yometa malirowo anthu amapangana kulonga mfumu ina.
Patsikuli amasonkhana anyakwawa, madoda, amayi, atsikana ndi anyamata.
Anyakwawa amafunsa amayi nati, ‘Mukuganiza kuti pamudzi pano amene angathe
kusunga anthu bwino ndani?’ Ndipo amayi amanena munthu amene angathe
kusunga mudzi, natchula monga ‘Kalichero’.
Kalicheroyo amayesa kukana mwina poopa abale ake kuti angamuphe chifukwa
cha ufumu. Dziwani kuti ufumu wa Achewa amalonga mphwake wa mfumu,
yemwe ali mwana wa mlongo wa mfumu, osati mwana kapena m’bale wake
monga imachitira mitundu ina. Akatero amayamba kuyimba nati, ‘Ponda, ye, ye,
ponda. Ponda, ye, ye, ponda.’
Atatha izi amayamba kulanga nati, ‘Lero mwakula, zachibwana lekani. Ngati
munali kuba, kuchita chigololo, kusewera ndi ana ndi zina zotere zonse muleke
lero.’ Mmenemo amayi akuombera m’manja, kuvomereza mawu onenedwawo kuti
ndioona ndiposo okhulupirika. Mfumuyi imauzidwa zonse zamasungidwe ena a
mudzi, monga kutsirika mudziwo kuti zilombo zisamafikemo. Ndipo anthu
amauzidwa kuti palibe mmodzi azati, ‘Kalichero,’ koma aliyense anene kuti,
‘Amfumu,’ kapena ‘Akathewera.’
Tsono mfumu yasopanoyi ngati ikufuna kuti pamudzipo pakhale muzinda poti
izimetera anamwali, imapita kwa mfumu yomwe imagulitsa mankhwala. Atagula
amafika kumudzi, natenga mankhwalawo pamodzi ndi mafuwa amene amayiwo
amayambira kuika pamowa wachinamwali.
78
Tsiku lina amasonkhana anamkungwi ndi amayi a midzi yoyandikana kudzavina
chinamwali. Dzina lachinamwali chotere amachicha ‘Chimbwinda’; ndiko kuti ali
ndi pakati chinamwali asanachite.
Amayi amasonkhana kunyumba kwa namwaliyo, nayamba kumvula zovala zonse
ndi kumulola kuvala m’chiuno mokha. Panthawiyi mimba yonse ili poyera.
Amachita ichi kuti mfumu ndi ena onse aone mimbayo. Atatero namwaliyo
amatengedwa napita naye ku mtengo wa anamwali kuti akam’vinire.
Mfumuyo podwala, nduna zake pamodzi ndi amayi amapita kwa woombeza ula.
Atafika waulayo amati, ‘Moni nonse. Nanga mwasiya kwa bwino ku mudzi?’
Amayankha nati, ‘Ife tasiya matenda, ndipo tatsata inu kuti mutidziwitse chimene
mfumuyo yadwalira.’
Zitamva izi, ndunazo, zimapita kumudzi nafotokoza zonse ndi kuti ula wagwira
uje. ‘Akuti adaika mankhwala pa khomo, ndipo ngati mankhwalawo sachotsedwa
mfumuyi ifa.’ Amafunafuna mankhwalawo koma osawapeza. Kwa iye amene ula
wam’gwera amakhala ndi nkhawa poziwa kuti ali ndi mlamndu ngati mfumu
yamwalira. Koma amachitanso mantha kutsutsa waulayo. Aula amanena zambiri
koma zosachitika; mwina amati mukapeza wodwalayo atamwalira, koma mwina
amamupeza wamoyo nachira.
79
Nthawi zonse mkazi akatha msinku, kuyambira pamenepo amathawana ndi mfumu
mpaka tsiku lachinamwali chake. Koma muja amati masiku sakoma onse,
mwadzidzidzi mfumuyo imatupa miyendo ndipo anthu amaganiza kuti mnyamata
amene adachita chimbwinda chija ndi amene adula mfumu. Nduna ya m’mudzi
imatuma anyamata okanena kwa mfumu imene idali nkhonswe ya mfumu polonga
mfumuyo ndiponso kwa mafumu ena onse.
Anthu ali kumanda, amafika mafumu a midzi ina ndi anyamata awo nachita
mputho, ndiko kuti atha kupha munthu aliyense am’peze, ndiponso zoweta
zilizonse popeza amapha chilichonse chimene akumana nacho, kotero anthu ambiri
amathawa. Ichi ndicho chifukwa chake katundu pamodzi ndi ana amachotsedwa,
kuopetsa mpunthowo. Ophedwawo amakhala mtsamiro wa mfumu. Zikuchitika
zimenezi nyawunso zimakhala zili lakalaka uku ndi uko. Ndipo akazi amakhala
otanganidwa kwambiri kuononga zinthu za mfumu yomwalirayo, monga
chimanga, chuma cham’nyumbamo, ndi zina zilizonse zopezeka m’nyumbamo.
Poika malirowo mwina amaika patapita masiku awiri, kuti amuna athe ku kumba
manda akuya kwambiri. Mtembo umanyamulidwa ndi nyawu izi:
Chabwerachaona, Ngangande, Njovu ndi Jere. Akazi samaonera maikidwe amaliro
amfumu. Katundu wina wam’nyumba amaikidwa pamodzi ndi ophedwa awiri
kapena anayi aja. Koma namwali okongora amaikidwa wa moyo kuti afukate
mfumu pa miyendo yake. Namwaliriyo amalira kufuna kutuluka koma kosatheka
kutero, amakwiridwa m’manda. Ndipo namwaliyo amamwalira polephera kupuma.
Nyau zimayamba tsiku lomwelo kuvina mpaka tsiku lotuluka pamtanda. Mfumuyo
ikamwalira akazi ake onse amatchedwa ‘aferekazi’, kutanthauza kuti anafedwa
aakazi. Akaziwo pamodzi ndi ana amathira dothi m’mandamo, chidzindikiro
chotsadzikana. Amatero kuopa mzimu wa wakufayo kuti ungadzafike ndikuvutitsa
abale, akazi ndi ana ake.
80
Atatuluka pamtanda, aferekazi amasambitsidwa nametedwa koyamba. Ndipo
zikatha izi aferekaziwo saloledwa kusamba thupi lonse, koma m’manja mokha
mpaka pa tsiku lometa kachiwiri; patapita zaka ziwiri. Chaka choyamba
mafumuwo amaphikitsa mowa kuti aone adzukulu ndi aferekaziwo. Panthawiyi
amasonkhana anthu ndi nyawu zochokera m’midzi yozungulira, navina masiku,
ndipo pa tsiku lotsiriza, aferekazi amaonana ndi adzukulu. Mowa umenewu
umatchedwa ‘sambiram’maso’. Ndiko kuti ayembekezanso mowa wina
wodzasambira thupi lonse ndi kumeta tsitsi lotsiriza.
Patsiku lometa maliro, patapita chaka, amafika mafumu ndi anthu ena. Ndipo
nyawu zimayamba kuvina tsiku lopola mowa kulekeza tsiku loshambula mowawo.
Patsiku loshambula pamafika nyawu zovina masana ndi usiku. Zilombo za masana
ndizo: Kadyankhanze, Simoni, Kachipapa, Chisambwe, Makanja, Pedegu, Njovu
ndi Jere. Zimenezi ndizo nyau zazikulu zomwe sizingafike pamaliro aliwonse,
koma pa chinamwali, maliro anamkungwi ndi maliro amfumu, basi.
81
Ngati aferekazi ndi ambiri, amphwake a mfumu amalimbirana akaziwo. Ngati
mfumukazi yatengedwa ndi mphwake wa mfumu, uyu samapereka chipindatchika,
koma mphwake wamfumu, womutengayo.
82
Patsogolo Kasiyamaliro ndi Mjere uja amabwerera kuti nawonso akavine
pawokha, ndiye nyimbo yake amadziyimbira namati, “Nyama?” Wothirira amati,
“Nyama yakwera mtunda, yasiya alenje.”
Makanja
Mochedwa dzuwa likulowa, gule yense atavina amakhala mathero azonse, anthu
n’kumang’ondokana. Usiku wotsatira ndilo tsiku lamchezo. Usiku wonse
kumakhala kuchezera kuyimba mpaka kufikira mbembembe kucha.
83
Ng’ombe
Malo olangira mfumu yatsopano akakonzedwa anthu onse monga mafumu, ndoda,
ntchembere, asungwana ndiponso anyamata amadza kufupi ndi bwalo. Poyamba
wolowa kuka ndiye amautsa nati, “Timverane.” Onse n’kuvomera akuomba
m’manja kuti bo, bo, bo. “Ayi ndaimirachi n’kuti tsopano tilange mfumu yathu.
Ndiye pano tikhale omasuka kunenapo chomwe mudziwa pamakhalidwe a
mfumuyi, oipa kapena abwino.”
Nyimbo inanso imati, “Mudzi ukamanga umakhala bwino ndi wana, ayee,
kuyankhula kuja udzaleke, ayee, mwakula lero mwakula.”
84
Mawu otsiriza
Zikomo.
Mwini Mtunda
Dziko lidagawidwa motere;
1. Dziko(Area) ndi gawo loyang’aniridwa ndi Traditional Authority(Chief).
2. Mkati mwa dziko muli zigawo ndizo Mtunda. Mmenemu woyang’anira wake
amati Mwini Mtunda.
3. Palinso gawo lina ndilo Mudzi, ndipo woyang’anira wake amati Mfumu kapena
Nyakwawa (Village Headman). Ntchito yake ndikuyang’anira Nzika kapena
Mbadwa za m’mudzimo.Mfumuyi imapatsidwa malo ndi Mwini Mtunda.
Wopempha malo amatchedwa Mbiri, atawapeza a Mfumu amafunsindwa
85
cholinga chake, ndipo iye amati, ‘Palibe, ndilikufuna malo okhalapo.” Mwini
Mtunda amanyamuka nakam’lozera dela limene azakhalepo.
86